Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 74:2 - Buku Lopatulika

2 Kumbukirani msonkhano wanu, umene munaugula kale, umene munauombola ukhale fuko la cholowa chanu; Phiri la Ziyoni limene mukhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Kumbukirani msonkhano wanu, umene munaugula kale, umene munauombola ukhale fuko la cholandira chanu; Phiri la Ziyoni limene mukhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Kumbukirani mpingo wanu umene mudaupatula kuyambira kale, mtundu umene Inu mudauwombola kuti ukhale wanuwanu. Kumbukirani phiri la Ziyoni kumene Inu mudadzakhala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale, fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola, phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 74:2
27 Mawu Ofanana  

Potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ake, nanyansidwa Iye ndi cholowa chake.


Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo, Israele, akhale chuma chake chenicheni.


Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao; mtundu womwe anausankha ukhale cholowa cha Iye yekha.


Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.


Munaombola anthu anu ndi mkono wanu, ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.


Imbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni; lalikirani mwa anthu ntchito zake.


Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira; saiwala kulira kwa ozunzika.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholowa chake.


Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola; mwamphamvu yanu mudawalondolera njira yakunka pokhala panu poyera.


Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola.


Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.


Ndipo iwo adzawatcha Anthu opatulika, Oomboledwa a Yehova; ndipo iwe udzatchedwa Wofunidwa, Mzinda wosasiyidwa.


Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete,


Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.


M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.


Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndi mtundu wa cholowa chake, dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.


Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake.


Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.


Ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuti, Yehova Mulungu, musaononga anthu anu ndi cholowa chanu, amene mudawaombola mwa ukulu wanu, amene munawatulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Koma iwo ndiwo anthu anu ndi cholowa chanu, amene mudawatulutsa ndi mphamvu yanu yaikulu ndi dzanja lanu lotambasuka.


amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa