Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 74:1 - Buku Lopatulika

1 Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu Mulungu, chifukwa chiyani mukutitaya mpaka muyaya? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutirira nkhosa za busa lanu ngati moto?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 74:1
30 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzataya chotsala cha cholowa changa, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo chakudya ndi chofunkha cha adani ao onse;


Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso?


Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake.


Unakwera utsi wotuluka m'mphuno mwake, ndi moto wa m'kamwa mwake unanyeka nuyakitsa makala.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.


Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?


Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa; ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu.


Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.


Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; mwakwiya; tibwezereni.


Si ndinu, Mulungu, amene mwatitaya? Osatuluka nao makamu athu, Mulungu.


Kodi Ambuye adzataya nthawi yonse? Osabwerezanso kukondwera nafe.


Chifundo chake chalekeka konsekonse kodi? Lonjezano lake lidatha kodi ku mibadwo yonse?


Tamverani, anthu anga, chilamulo changa; tcherezani khutu lanu mau a pakamwa panga.


Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu tidzakuyamikani kosatha; tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.


Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti? Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?


Munawadyetsa mkate wa misozi, ndipo munawamwetsa misozi yambiri.


Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?


Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!


Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?


Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.


Tsoka abusa amene athetsa nabalalitsa nkhosa za busa langa! Ati Yehova.


Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzachotsa mbeu zonse za Israele chifukwa cha zonse anazichita, ati Yehova.


Koma mwatikaniza konse, mwatikwiyira kopambana.


Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.


Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakuthengo, chifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunefune nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;


Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.


Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa