Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 77:8 - Buku Lopatulika

8 Chifundo chake chalekeka konsekonse kodi? Lonjezano lake lidatha kodi ku mibadwo yonse?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chifundo chake chalekeka konsekonse kodi? Lonjezano lake lidatha kodi ku mibadwo yonse?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Kodi chikondi chao chosasinthika chija chatheratu? Kodi malonjezo ao aja atha mpaka muyaya?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu? Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 77:8
11 Mawu Ofanana  

Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.


Ndidzachita uphungu m'moyo mwanga kufikira liti, pokhala ndi chisoni m'mtima mwanga tsiku lonse? Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti?


Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?


Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?


Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.


Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?


Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga chaka chimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa.


Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?


Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;


Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa