Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 77:9 - Buku Lopatulika

9 Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo? Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo? Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Kodi Mulungu waiŵala kukoma mtima kwake kuja? Kodi wakwiya ndi kuleka chifundo chake chija?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima? Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 77:9
10 Mawu Ofanana  

Kumbukirani, Yehova, nsoni zanu ndi chifundo chanu; pakuti izi nza kale lonse.


Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.


Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.


Bwanji iwe, Yakobo, umati, ndi bwanji umanena iwe, Israele, Njira yanga yabisika kwa Yehova; ndipo chiweruzo cha Mulungu wanga chandipitirira?


Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?


Pakuti Mulungu anatsekera pamodzi onse m'kusamvera, kuti akachitire onse chifundo.


Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa