Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 77:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo ndinati, Chindiwawa ichi; koma ndikumbukira zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo ndinati, Chindilaka ichi; koma ndikumbukira zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Chondiŵaŵa ndi chakuti, Mulungu Wopambanazonse wasintha mchitidwe wake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso: zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 77:10
12 Mawu Ofanana  

Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu? Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikire, zondidabwitsa, zosazidziwa ine.


Pofulumizidwa mtima ndinati ine, anthu onse nga mabodza.


Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.


ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu.


Ndinaganizira masiku akale, zaka zakalekale.


Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.


Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


Pomwepo atate wa mwana anafuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.


Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa