Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Masalimo 4:4 - Buku Lopatulika Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Opani Mulungu, ndipo musachimwe. Mukhale phee ndipo muganize zimenezi mu mtima pamene mukugona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwiyani koma musachimwe; pamene muli pa mabedi anu, santhulani mitima yanu ndi kukhala chete. Sela |
Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa; wosunga njira yake atchinjiriza moyo wake.
Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.
Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.
Dziyeseni nokha, ngati muli m'chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Mukapanda kukhala osatsimikizidwa.