Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.
Masalimo 24:4 - Buku Lopatulika Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake, ndipo amaganiza zabwino mumtima mwake. Ndi amene salingalira zonama, ndipo salumbira monyenga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera, amene sapereka moyo wake kwa fano kapena kulumbira mwachinyengo. |
Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.
Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.
Yehova anandibwezera monga mwa chilungamo changa; anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.
Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?
wosadya pamapiri, kapena kukweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake,
wosadya pamapiripo, wosakweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake, kapena kuyandikira mkazi ataoloka,
Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.
nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.
ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.
achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;
Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.