Masalimo 24 - Buku LopatulikaUlemerero wa Yehova Salimo la Davide. 1 Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo. 2 Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi. 3 Adzakwera ndani m'phiri la Yehova? Nadzaima m'malo ake oyera ndani? 4 Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga. 5 Iye adzalandira dalitso kwa Yehova, ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake. 6 Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye, iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo. 7 Weramutsani mitu yanu, zipata inu; ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha, kuti Mfumu ya ulemerero ilowe. 8 Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wamphamvu ndi wolimba, Yehova wolimba kunkhondo. 9 Weramutsani mitu yanu, zipata inu; inde weramutsani, zitseko zosatha inu, kuti Mfumu ya ulemerero ilowe. 10 Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wa makamumakamu, ndiye Mfumu ya ulemerero. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi