Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.
Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala.
Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife.
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;
Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.