Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 66:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Inu Mulungu, mwatiyesa, mwatiyeretsa monga m'mene amayeretsera siliva.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pakuti Inu Mulungu munatiyesa; munatiyenga ngati siliva.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 66:10
11 Mawu Ofanana  

Koma adziwa njira ndilowayi; atandiyesa ndidzatuluka ngati golide.


Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.


Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng'anjo; koma Yehova ayesa mitima.


Chotsera siliva mphala yake, mmisiri wa ng'anjo atulutsamo mbale.


Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golide ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m'chilungamo.


musamamvera mau a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu; popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziwe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.


amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;


Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa