Zekariya 13:9 - Buku Lopatulika9 Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Anthu a m'chigawo chachitatuchi ndidzaŵaika pa moto, ndidzaŵayeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Ndidzaŵayesa monga m'mene amayesera golide. Tsono adzatama dzina langa mopemba, Ine mwiniwake nkuŵayankha. Ndidzanena kuti, ‘Ameneŵa ndi anthu anga.’ Iwowo adzati, ‘Chauta ndi Mulungu wathu.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto; ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide. Adzayitana pa dzina langa ndipo Ine ndidzawayankha; Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’ ” Onani mutuwo |