Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 14:1 - Buku Lopatulika

1 Taonani likudza tsiku la Yehova, limene zofunkha zako zidzagawanika pakati pako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Taonani likudza tsiku la Yehova, limene zofunkha zako zidzagawanika pakati pako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Onani, tsiku likubwera, la Chauta, pamene zinthu zomwe adani ako adakulanda, azidzagaŵana iwe uli pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Taonani tsiku la Yehova likubwera pamene zinthu zimene adani ako anakulanda azidzagawana iwe ukuona.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 14:1
12 Mawu Ofanana  

Kuwani inu; pakuti tsiku la Yehova lili pafupi; lidzafika monga chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.


Taonani tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali; kupasula dziko, ndi kudzaonongamo akuchimwa psiti.


Chifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;


Muombe lipenga mu Ziyoni, nimufuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira;


Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.


Aunyinji, aunyinji m'chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m'chigwa chotsirizira mlandu.


Khala chete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ake.


Ndi Yuda yemwe adzachita nkhondo ku Yerusalemu; ndi zolemera za amitundu onse ozungulirapo zidzasonkhanitsidwa, golide, ndi siliva, ndi zovala zambirimbiri.


Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.


Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.


dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera.


pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa