Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 80 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 80

Apempha Mulungu alanditse anthu ake m'chisautso chao
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Syosyanimu; lochita mboni. Salimo la Asafu.

1 Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.

2 Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase, ndipo mutidzere kutipulumutsa.

3 Mutibweze, Mulungu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

4 Yehova, Mulungu wa makamu, mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti?

5 Munawadyetsa mkate wa misozi, ndipo munawamwetsa misozi yambiri.

6 Mutiika kuti atilimbirane anzathu; ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha.

7 Mulungu wa makamu, mutibweze; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

8 Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito, munapirikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.

9 Mudasoseratu pookapo, idagwiritsa mizu yake, ndipo unadzaza dziko.

10 Mthunzi wake unaphimba mapiri, ndi nthambi zake zikunga mikungudza ya Mulungu.

11 Unatambalitsa mphanda zake mpaka kunyanja, ndi mitsitsi yake kufikira ku Mtsinje.

12 Munapasuliranji maphambo ake, kotero kuti onse akupita m'njira atcherako?

13 Nguluwe zochokera kuthengo ziukumba, ndi nyama za kuchidikha ziudya.

14 Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu; suzumirani muli m'mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,

15 ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka, ndi mphanda munadzilimbikitsira.

16 Unapserera ndi moto, unadulidwa; aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.

17 Dzanja lanu likhale pa munthu wa padzanja lamanja lanu; pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.

18 Potero sitidzabwerera m'mbuyo kukusiyani; titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu.

19 Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi