Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 80:9 - Buku Lopatulika

9 Mudasoseratu pookapo, idagwiritsa mizu yake, ndipo unadzaza dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mudasoseratu pookapo, idagwiritsa mizu yake, ndipo unadzaza dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Mudaulimira munda mpesawo, udamera mizu yozama, nudzaza m'dzikolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Munawulimira munda wamphesawo, ndipo unamera ndi kudzaza dziko.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 80:9
17 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawavutanso, monga poyamba paja,


Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.


Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.


Ndipo Yowabu anapereka kwa Davide chiwerengo cha anthu owerengedwa. Ndipo Aisraele onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga.


Ndipo anawapatsa maiko a amitundu; iwo ndipo analanda zipatso za ntchito ya anthu:


Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,


Tsiku limenelo: munda wa mphesa wavinyo, imbani inu za uwo.


M'mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israele adzaphuka ndi kuchita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso padziko lonse lapansi.


Ndipo otsala amene opulumuka a nyumba ya Yuda adzaphukanso mizu pansi, nadzabala chipatso pamwamba.


ndipo iye anakumba mcherenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pake nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.


Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patali ndi impso zao.


Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?


Ndipo ndinatuma mavu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa