Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 80:17 - Buku Lopatulika

17 Dzanja lanu likhale pa munthu wa padzanja lamanja lanu; pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Dzanja lanu likhale pa munthu wa pa dzanja lamanja lanu; pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Koma ndi dzanja lanu muteteze anthu amene mudaŵasankha, anthu amene Inu nomwe mwaŵalimbikitsa kuti akutumikireni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja, mwana wa munthu amene mwalera nokha.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 80:17
8 Mawu Ofanana  

Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka, ndi mphanda munadzilimbikitsira.


Amene dzanja langa lidzakhazikika naye; inde mkono wanga udzalimbitsa.


Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.


Yehova anatcha dzina lako, Mtengo wa azitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikulu wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zake zathyoka.


nuziti kwa dziko la Israele, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'chimake, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa