Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 80:19 - Buku Lopatulika

19 Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale. Mutiwonetse nkhope yoŵala, kuti ife tipulumuke.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 80:19
11 Mawu Ofanana  

Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.


Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.


Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu, mundipulumutse ndi chifundo chanu.


Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,


Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.


Mutibweze, Mulungu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.


Mulungu wa makamu, mutibweze; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.


ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.


Potero muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja.


Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipatukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa