Numeri 14:11 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi anthu ameneŵa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzaleka liti kusandikhulupirira, ngakhale aone zizindikiro zimene ndachita pakati pao? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anawuza Mose kuti, “Anthu awa adzandinyoza mpaka liti? Sadzandikhulupirira mpaka liti, ngakhale ndachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi pakati pawo? |
Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti?
Musamalire iye, ndi kumvera mau ake; musamuwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa lili m'mtima mwake.
Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?
Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.
Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?
Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.
Mwanawang'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?
Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleke;
sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona;
Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israele, amene amandidandaulira.
Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno.
Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.
Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate.
Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso.
Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adatuluka mu Ejipito ndi Mose?
musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo, monga muja tsiku la chiyesero m'chipululu,