Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 3:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wake?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wake?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Nanga Mulungu ankanena za yani pamene adaati, “Ndikulumbira kuti ameneŵa sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera?” Pajatu ankanena za anthu amene adaamuukira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Nanga Mulungu ankanena za ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Pajatu ankanena za anthu amene sanamvere aja.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 3:18
16 Mawu Ofanana  

Popeza sanakhulupirire Mulungu, osatama chipulumutso chake.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?


sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona;


simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.


amuna amene anaipsa mbiri ya dziko, anafa ndi mliri pamaso pa Yehova.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Popeza simunandikhulupirira Ine, kundipatula Ine pamaso pa ana a Israele, chifukwa chake simudzalowetsa msonkhano uwu m'dziko ndinawapatsali.


Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.


Pakuti monga inunso kale simunamvere Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo mwa kusamvera kwao,


Ndipo pamene Yehova anakutumizani kuchokera ku Kadesi-Baranea, ndi kuti Kwerani, landirani dziko limene ndakupatsani; munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu, osamkhulupirira, kapena kumvera mau ake.


Monga ndinalumbira mu ukali wanga: Ngati adzalowa mpumulo wanga!


Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.


Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindule nao mau omvekawo, popeza sanasakanizike ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.


Popeza tsono patsala kuti ena akalowa momwemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa iwo kale sanalowemo chifukwa cha kusamvera,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa