Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 3:17 - Buku Lopatulika

17 Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Nanga amene Mulungu adaaŵakwiyira zaka makumi anai, ndani? Ndi anthu amene adaachimwa aja, mitembo yao nkutsalira m'chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Nanga amene Mulungu anawakwiyira zaka makumi anayi anali ndani? Kodi si anthu amene anachimwa, amene mitembo yawo inatsala mʼchipululu muja?

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 3:17
11 Mawu Ofanana  

Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.


Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga chipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wochitola.


popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;


Nunene nao, Pali Ine ati Yehova, ndidzachitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga;


mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwani konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;


amuna amene anaipsa mbiri ya dziko, anafa ndi mliri pamaso pa Yehova.


Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa