Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 3:16 - Buku Lopatulika

16 Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adatuluka mu Ejipito ndi Mose?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adatuluka m'Ejipito ndi Mose?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Nanga amene adaamva mau ake a Mulungu namuukira, ndani? Ndi onse aja amene Mose adaaŵatsogolera nkuŵatulutsa m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto?

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 3:16
18 Mawu Ofanana  

Koma anaonjeza kumchimwira Iye, kupikisana ndi Wam'mwambamwamba m'chipululu.


Kawirikawiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako, nammvetsa chisoni m'chipululu.


ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.


chifukwa cha choipa chao anachichita kuutsa nacho mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu ina, imene sanaidziwe, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.


popeza muutsa mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu, pofukizira milungu ina m'dziko la Ejipito, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale chitemberero ndi chitonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi?


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao?


Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno!


koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo.


simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.


Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.


Ndipo anati wina ndi mnzake, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Ejipito.


Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.


Yoswa mwana wa Nuni, wakuima pamaso pako, iye adzalowamo; umlimbitse mtima; popeza iye adzalandiritsa Israele.


Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa