Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 3:19 - Buku Lopatulika

19 Si awo kodi osamverawo? Ndipo tiona kuti sanathe kulowa chifukwa cha kusakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Si awo kodi osamverawo? Ndipo tiona kuti sanakhoza kulowa chifukwa cha kusakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Motero tikuwona kuti anthuwo sadathe kuloŵa, chifukwa cha kusakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Tsono ife tikuona kuti sanalowe chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 3:19
10 Mawu Ofanana  

Anapeputsanso dziko lofunika, osavomereza mau ake;


Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.


Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupirira waweruzidwa ngakhale tsopano, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.


Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.


Ndipo iwonso, ngati sakhala chikhalire mu kusakhulupirira, adzawalumikizanso, pakuti Mulungu ali wamphamvu yakutha kuwalumikizanso.


Koma m'chinthu ichi simunakhulupirire Yehova Mulungu wanu,


kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirire choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama.


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirire umboni wa Mulungu anauchita wa Mwana wake.


Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa