Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 8:14 - Buku Lopatulika

14 Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleke;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleka;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Paja ndidaatsimikiza mtima kuti ndikuwonongeni, chifukwa chakuti makolo anu adaandikwiyitsa, ndipo sindidafune kukhululuka. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Monga ndinatsimikiza mtima kubweretsa choyipa pa inu, komanso osakuchitirani chisoni pamene makolo anu anandikwiyitsa,” akutero Yehova,

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 8:14
12 Mawu Ofanana  

koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.


Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire, zolingirira za m'mtima mwake ku mibadwomibadwo.


Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala;


Munthuyo akhale ngati mizinda imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;


Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.


Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzala, ati Yehova.


Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa choipa chonsechi, chomwecho ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonjeza.


Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.


Ine Yehova ndachinena, chidzachitika; ndipo ndidzachichita, sindidzamasula, kapena kulekerera, kapena kuwaleka, monga mwa njira zako, ndi monga umo unachitira adzakuweruza iwe, ati Ambuye Yehova.


Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu.


Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa