Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.
Nehemiya 1:6 - Buku Lopatulika mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsekulani maso ndipo tcherani khutu, kuti mumve pemphero la mtumiki wanune, limene ndikupereka tsopano kwa Inu usana ndi usiku, kupempherera Aisraele atumiki anu. Ndikuvomera machimo amene ife Aisraele tidakuchimwirani. Zoonadi, ine pamodzi ndi banja la makolo anga, tidakuchimwirani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tcherani khutu lanu ndi kutsekula maso anu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune limene ndikupemphera usana ndi usiku pamaso panu kupempherera Aisraeli, atumiki anu. Ndikuvomereza machimo a Aisraeli amene tinakuchimwirani. Ndithu, ine ndi banja la makolo anga tinakuchimwirani. |
Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.
ndipo akakumbukira mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza Inu m'dziko iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tachimwa, ndipo tachita mphulupulu, tachita moipa;
Ndipo tsopano mukuti mugonjetse ana a Yuda ndi Yerusalemu akhale akapolo ndi adzakazi anu; palibe nanunso kodi milandu yopalamula kwa Yehova Mulungu wanu?
Pakuti analakwa makolo athu, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu, namsiya, natembenuza nkhope zao osapenya chokhalamo Yehova, namfulatira.
Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale chipenyere, ndi makutu anu chimvere, pemphero lochitika pamalo pano.
Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu.
Chifukwa chake tsono, wululani kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, nimuchite chomkondweretsa; mudzilekanitse ndi mitundu ya anthu a m'dzikomo, ndi kwa akazi achilendo.
Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.
Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.
Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m'dziko la Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tachimwa, tachita choipa.
Ndipo pakunena ine, ndi kupemphera, ndi kuvomereza tchimo langa, ndi tchimo la anthu a mtundu wanga Israele, ndi kutula chipembedzero changa pamaso pa Yehova Mulungu wanga, chifukwa cha phiri lopatulika la Mulungu wanga;
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,
tachimwa, tachita mphulupulu, tachita zoipa, tapanduka, kupatuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu;
Yehova, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takuchimwirani.
Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?
zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.
amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;
Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.
Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,
Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.
Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.