Ezara 10:1 - Buku Lopatulika1 Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pamene Ezara ankapemphera ndi kulapa, alikulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, chinamtindi cha anthu chidabwera kwa iye kudzasonkhana. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera m'dziko lonse la Israele, ndipo ankalira koopsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Pamene Ezara ankapemphera ndi kuvomereza tchimo lawo, akulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, anthu ambiri anabwera kwa iye kudzasonkhana naye. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera mʼdziko lonse la Israeli ndipo ankalira kwambiri. Onani mutuwo |