Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 106:6 - Buku Lopatulika

6 Talakwa pamodzi ndi makolo athu; tachita mphulupulu, tachita choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Talakwa pamodzi ndi makolo athu; tachita mphulupulu, tachita choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ife tachimwa monga makolo athu, tachita zoipa, sitidachite zabwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu; tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 106:6
14 Mawu Ofanana  

ndipo akakumbukira mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza Inu m'dziko iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tachimwa, ndipo tachita mphulupulu, tachita moipa;


Ndipo tsopano, Mulungu wathu, tidzanenanji pambuyo pa ichi? Pakuti tasiya malamulo anu,


Tachita mwamphulupulu pa Inu, osasunga malamulo, kapena malemba, kapena maweruzo, amene mudalamulira mtumiki wanu Mose.


Koma iwo ndi makolo athu anachita modzikuza, naumitsa khosi lao, osamvera malamulo anu,


Ndi kuti asange makolo ao, ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wao, ndi mzimu wao sunakhazikike ndi Mulungu.


Tivomereza, Yehova, chisalungamo chathu, ndi choipa cha makolo athu; pakuti takuchimwirani Inu.


Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvere mau a Yehova Mulungu wathu.


Pamenepo adzavomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pochita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,


Ndipo taonani, mwauka m'malo mwa makolo anu, gulu la anthu ochimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israele.


Dzazani inu muyeso wa makolo anu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa