Nehemiya 1:11 - Buku Lopatulika11 Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Yehova, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Inu Chauta, tcherani khutu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu ena amene amakonda kulemekeza dzina lanu. Lolani kuti ine mtumiki wanu zinthu zindiyendere bwino lero, ndipo kuti mfumu indichitire chifundo.” Pa nthaŵi imeneyo nkuti ine ndili woperekera zakumwa kwa mfumu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Inu Ambuye tcherani khutu lanu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu amene amakondwera kuchitira ulemu dzina lanu. Lolani kuti mtumiki wanune zinthu zindiyendere bwino lero ndi kuti mfumu indichitire chifundo.” Nthawi imeneyi nʼkuti ndili woperekera zakumwa kwa mfumu. Onani mutuwo |