Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 5:7 - Buku Lopatulika

7 Atate athu anachimwa, kulibe iwo; ndipo tanyamula mphulupulu zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Atate athu anachimwa, kulibe iwo; ndipo tanyamula mphulupulu zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Makolo athu adachimwa, ndipo adatha. Ndiye ife tatengana nacho chilango chifukwa cha machimo ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Makolo athu anachimwa ndipo anafa kale, koma chilango chawo chili pa ife.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 5:7
15 Mawu Ofanana  

Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.


Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.


Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.


Diso la amene andiona silidzandionanso, maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.


Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;


Tivomereza, Yehova, chisalungamo chathu, ndi choipa cha makolo athu; pakuti takuchimwirani Inu.


Pamenepo uziti kwa iwo, Chifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu ina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga chilamulo changa;


ndipo mwachita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wake woipa, kuti musandimvere Ine;


Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.


Masiku omwewo sadzanenanso, Atate adya mphesa zowawa, ndi mano a ana ayayamira.


Wasenza choipa chako ndi zonyansa zako, ati Yehova.


Mutani inu ndi kunena mwambi uwu za dziko la Israele, wakuti, Atate adadya mphesa zosacha, ndi mano a ana ayayamira.


Makolo anu, ali kuti iwowo? Ndi aneneri, akhala ndi moyo kosatha kodi?


Yehova ndiye wolekereza, ndi wa chifundo chochuluka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula wopalamula; wakuwalanga ana chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa