1 Samueli 15:11 - Buku Lopatulika11 Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 “Ndikumva chisoni kuti ndidampatsa ufumu Saulo. Wabwerera m'mbuyo, waleka kunditsata, ndipo sadamvere malamulo anga.” Pamenepo Samuele adapsa mtima, ndipo adadandaula kwa Chauta usiku wonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 “Ine ndikumva chisoni chifukwa ndinayika Sauli kukhala mfumu. Wabwerera mʼmbuyo, waleka kunditsata ndipo sanamvere malangizo anga.” Samueli anapsa mtima, ndipo analira kwa Yehova usiku wonse. Onani mutuwo |
Koma wolungamayo akabwerera kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, ndi kuchita monga mwa zonyansa zonse azichita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena chimodzi cha zolungama zake zonse adzazichita chidzakumbukika m'kulakwa kwake analakwa nako, ndi m'kuchimwa kwake anachimwa nako; momwemo adzafa.