Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 88:1 - Buku Lopatulika

1 Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa, ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa, ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu Chauta, Mpulumutsi wanga, ndimalirira Inu usana ndi usiku, kuti mundithandize.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa, usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 88:1
30 Mawu Ofanana  

Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova.


Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezara, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yake inafikira amitundu onse ozungulira.


Ndipo Solomoni anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lake, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomoni anapatsa Hiramu chaka ndi chaka.


Ndi ana a Zera: Zimiri, ndi Etani, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Dara; onse pamodzi ndi asanu.


Ndipo ana a Kohati ndiwo Amuramu, ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele.


mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.


Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa, munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.


Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza; ndipo usiku, sindikhala chete.


Iye adzalandira dalitso kwa Yehova, ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake.


Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?


Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.


Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.


Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.


Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino.


Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.


Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo, Mulungu wa chipulumutso chathu; ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi, ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.


Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.


Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu, chifukwa cha dzina lanu.


Mundichitire chifundo, Ambuye; pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.


Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.


Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete,


ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,


Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?


chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu,


zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.


ndi kuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa chikhulupiriro chanu?


Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,


osatapa pa zao, komatu aonetsere chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse.


akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa