Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Timoteyo 1:3 - Buku Lopatulika

3 Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbu mtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndikuthokoza Mulungu amene ndimamtumikira ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, monga momwe ankachitira makolo anga. Ndimamthokoza ndikamakukumbukira kosalekeza m'mapemphero anga usana ndi usiku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga.

Onani mutuwo Koperani




2 Timoteyo 1:3
21 Mawu Ofanana  

zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.


Ine ndine munthu Myuda, wobadwa mu Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;


Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu a milandu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.


Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;


M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.


Mayendedwe a moyo wanga tsono, kuyambira pa chibwana changa, amene anakhala chiyambire mwa mtundu wanga mu Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse;


Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira,


Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.


sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m'mapemphero anga;


ndi kuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa chikhulupiriro chanu?


ndi kukhala nacho chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma, chimene ena adachikankha, chikhulupiriro chao chidatayika;


koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m'chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga;


Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.


pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa agogo ako Loisi, ndi mwa mai wako Yunisi, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.


ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.


Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa