Masalimo 67:1 - Buku Lopatulika Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa, atiwalitsire nkhope yake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa, atiwalitsire nkhope yake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa, mutiwunikire ndi chikondi chanu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire. |
Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholowa chanu; muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Landirani, Yehova, chotetezera anthu anu Israele, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosachimwa ukhale pakati pa anthu anu Israele; ndipo adzawatetezera cha mwaziwo.