Masalimo 42:1 - Buku Lopatulika Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi, kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu. |
Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.
Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.
Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.
Ndipo ana aamuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiyasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora.
Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;
ndi dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse.