Masalimo 45 - Buku LopatulikaNyimbo yoimbira ukwati wa mfumu Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Syosyanimu. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Nyimbo ya chikondi. 1 Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba. 2 Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu, chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha. 3 Dzimangireni lupanga lanu m'chuuno mwanu, wamphamvu inu, ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu. 4 Ndipo pindulani, mu ukulu wanu yendani, kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo; ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa. 5 Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu. 6 Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zomka muyaya. Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika. 7 Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa, chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu. 8 Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya; m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani. 9 Mwa omveka anu muli ana aakazi a mafumu; ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu wovala golide wa ku Ofiri. 10 Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako; uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako; 11 potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako, pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye. 12 Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu. 13 Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba, zovala zake nza malukidwe agolide. 14 Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga, anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu. 15 Adzawatsogolera ndi chimwemwe ndi kusekerera, adzalowa m'nyumba ya mfumu. 16 M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako, udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi. 17 Ndidzawakumbutsa dzina lanu m'mibadwomibadwo; chifukwa chake mitundu ya anthu idzayamika Inu kunthawi za nthawi. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi