Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 45:13 - Buku Lopatulika

13 Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba, zovala zake nza malukidwe agolide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba, zovala zake nza malukidwe agolide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 ndi chuma chao chamitundumitundu. Mwana wamkazi wa mfumu ali m'chipinda mwake, wadzikongoletsa kwambiri, wavala zovala zoluka ndi thonje lagolide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake, chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 45:13
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri;


Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata, mwana wamkaziwe wa mfumu! Pozinga m'chuuno mwako pakunga zonyezimira, ntchito ya manja a mmisiri waluso.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.


Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m'kati mwake?


Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.


koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.


ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;


Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.


Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa