Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 45:14 - Buku Lopatulika

14 Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga, anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga, anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Akupita naye kwa mfumu atavala zovala zamaluŵa, pamodzi ndi anamwali anzake omperekeza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu; anamwali okhala naye akumutsatira ndipo abweretsedwa kwa inu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 45:14
13 Mawu Ofanana  

Ndipo pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; nsichi zake zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.


Ndipo upikule malaya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika.


Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala zakuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini.


Bwenzi lako wapita kuti, mkaziwe woposa kukongola? Bwenzi lako wapatukira kuti, tikamfunefune pamodzi nawe?


Anati, Bwera, bwera, Msulamiwe; bwera, bwera, tiyang'ane pa iwe. Muyang'aniranji pa Msulami, ngati pa masewero akuguba?


Alipo akazi aakulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi, kudza akazi aang'ono makumi asanu ndi atatu, ndi anamwali osawerengeka.


Namwaliwe wokhala m'minda, anzako amvera mau ako: Nanenanso undimvetse.


Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.


Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.


Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera; chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa, nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa