Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 45:5 - Buku Lopatulika

5 Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mivi yanu ndi yakuthwa, imalasa mitima ya adani. Mitundu ina ya anthu imagwa pansi pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu, mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 45:5
18 Mawu Ofanana  

Pakuti mudzawabweza m'mbuyo, popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao.


Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Pakuti mivi yanu yandilowa, ndi dzanja lanu landigwera.


Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.


Mulungu amtulutsa mu Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake.


Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?


Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.


Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.


ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi;


Koma m'mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha.


Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha ophunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.


Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa