Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 45:17 - Buku Lopatulika

17 Ndidzawakumbutsa dzina lanu m'mibadwomibadwo; chifukwa chake mitundu ya anthu idzayamika Inu kunthawi za nthawi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndidzawakumbutsa dzina lanu m'mibadwomibadwo; chifukwa chake mitundu ya anthu idzayamika Inu kunthawi za nthawi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Ndidzamveketsa mbiri ku mibadwo yonse, nchifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse; choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 45:17
11 Mawu Ofanana  

Mafumu onse a padziko lapansi adzakuyamikani, Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.


Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi; ndiye wobadwa yekha wa amake; ndiye wosankhika wa wombala. Ana aakazi anamuona, namutcha wodala; ngakhale akazi aakulu a mfumu, ndi akazi aang'ono namtamanda.


Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.


Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa.


Iwe udzakhalanso korona wokongola m'dzanja la Yehova, korona wachifumu m'dzanja la Mulungu wako.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


Indetu ndinena kwa inu, kumene kulikonse Uthenga uwu Wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ichi chimene mkaziyo anachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake.


Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa