Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 45:10 - Buku Lopatulika

10 Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako; uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako; uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono mvera kuno, mkwati wamkaziwe, imva mau anga ndipo uŵaganizire bwino. Iŵala abale ako ndiponso nyumba ya bambo wako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu; iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 45:10
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;


Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.


Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golide matalente mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomoni.


Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga.


Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.


Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.


Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.


Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,


navule zovala za ukapolo wake, nakhale m'nyumba mwanu, nalire atate wake, ndi mai wake mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wake, ndi iye akhale mkazi wanu.


amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa