Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 45:9 - Buku Lopatulika

9 Mwa omveka anu muli ana aakazi a mafumu; ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu wovala golide wa ku Ofiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mwa omveka anu muli ana akazi a mafumu; ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu wovala golide wa ku Ofiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 ana aakazi a mafumu ali m'gulu la mbumba zanu zolemekezeka. Ku dzanja lanu lamanja kwaima mfumukazi, yovala zovala za golide wa ku Ofiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka; ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 45:9
19 Mawu Ofanana  

Ndipo zombo za Hiramu zotengera golide ku Ofiri zinatenganso ku Ofiri mitengo yambiri yambawa, ndi timiyala ta mtengo wapatali.


Tsono Bateseba ananka kwa mfumu Solomoni kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wake wachifumu, naikitsa mpando wina wa amake wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lake lamanja.


Ndipo tsono, usamuyesera iye wosachimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumchitira iye, nutsitsire mutu wake waimvi ndi mwazi kumanda.


ndi Ofiri, ndi Havila, ndi Yobabu. Awa onse ndiwo ana a Yokotani.


Ndipo utaye chuma chako kufumbi, ndi golide wa ku Ofiri ku miyala ya kumitsinje.


Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba, zovala zake nza malukidwe agolide.


Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.


ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira a mure ndi chisiyo ndi sinamoni.


Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata, mwana wamkaziwe wa mfumu! Pozinga m'chuuno mwako pakunga zonyezimira, ntchito ya manja a mmisiri waluso.


Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.


Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.


Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.


Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.


Ndipo amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwake; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.


Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa