Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 45:8 - Buku Lopatulika

8 Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya; m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya; m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Zovala zanu nzonunkhira mure, aloe ndi kasiya. Nyumba zanu zachifumu nzomangidwa ndi mnyanga. M'menemo zoimbira zansambo zimakusangalatsani,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya; kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 45:8
20 Mawu Ofanana  

Tsono machitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazichita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi mizinda yonse adaimanga, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; woongoka mtima adzapenya nkhope yake.


Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro.


Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.


Adzawatsogolera ndi chimwemwe ndi kusekerera, adzalowa m'nyumba ya mfumu.


Wokondedwa wanga mnyamatayo ali kwa ine ngati thumba la mure, logona pakati pa mawere anga.


Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.


Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo, wonunkhira ndi mure ndi lubani, ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?


Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, ndikamuka kuphiri la mure, ndi kuchitunda cha lubani.


Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi: Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga; ndadya uchi wanga ndi chisa chake; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi.


Masaya ake akunga chitipula chobzalamo ndiwo, ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira: Milomo yake ikunga akakombo, pakukhapo madzi a mure.


Ndinauka ndikatsegulire bwenzi langa; pamanja panga panakha mure. Ndi pa zala zanga madzi a mure, pa zogwirira za mpikizo.


Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa; ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.


Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.


M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo.


Koma anadzanso Nikodemo, amene anadza kwa Iye usiku poyamba paja, alikutenga chisakanizo cha mure ndi aloe, monga miyeso zana.


Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa