Masalimo 47 - Buku LopatulikaMau a kulemekeza Mulungu mwini dziko lonse lapansi Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la ana a Kora. 1 Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu; fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa. 2 Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi. 3 Atigonjetsera anthu, naika amitundu pansi pa mapazi athu. 4 Atisankhira cholowa chathu, chokometsetsa cha Yakobo amene anamkonda. 5 Mulungu wakwera ndi mfuu, Yehova ndi liu la lipenga. 6 Imbirani Mulungu, imbirani; imbirani mfumu yathu, imbirani. 7 Pakuti Mulungu ndiye mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani ndi chilangizo. 8 Mulungu ndiye mfumu ya amitundu, Mulungu akhala pa mpando wachifumu wake woyera. 9 Akulu a anthu asonkhana akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu; akwezeka kwakukulu Iyeyo. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi