Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 47:8 - Buku Lopatulika

8 Mulungu ndiye mfumu ya amitundu, Mulungu akhala pa mpando wachifumu wake woyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Mulungu ndiye mfumu ya amitundu, Mulungu akhala pa mpando wachifumu wake woyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mulungu amalamulira mitundu ya anthu. Mulungu amakhala pa mpando wake woyera waufumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 47:8
18 Mawu Ofanana  

Kukondwerere kumwamba, ndi dziko lapansi lisekerere; anene mwa amitundu, Yehova achita ufumu.


Adzaweruza mwa amitundu, adzadzaza dziko ndi mitembo; adzaphwanya mitu m'maiko ambiri.


Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.


Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wanu wachifumu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.


Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga; mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama.


Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.


Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo?


Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.


Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere; zisumbu zambiri zikondwerere.


Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.


Yehova ndiye wamkulu mu Ziyoni; ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.


Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lake ilo lokha.


Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.


Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.


Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa