Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 47:9 - Buku Lopatulika

9 Akulu a anthu asonkhana akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu; akwezeka kwakukulu Iyeyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Akulu a anthu asonkhana akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu; akwezeka kwakukulu Iyeyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Atsogoleri a anthu a mitundu ina yonse amasonkhana pamodzi ndi anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu onse a pansi pano ndi ake a Mulungu, Iyeyo ndiye wamkulu kopambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana monga anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu; Iye wakwezedwa kwakukulu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 47:9
21 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.


Inde mafumu onse adzamgwadira iye, amitundu onse adzamtumikira.


Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova; ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele.


Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.


Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.


Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu.


Mau onse a Mulungu ali oyengeka; ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.


Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.


Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.


Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Ine ndili Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo? Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo.


Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;


Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa