Masalimo 26:7 - Buku Lopatulika kuti ndimveketse mau a chiyamiko, ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti ndimveketse mau a chiyamiko, ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimaimba molimbika nyimbo yothokozera, ndimalalika ntchito zanu zonse zodabwitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kulengeza mofuwula za matamando anu ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa. |
Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.
Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu.
Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.
Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye;