Afulumizidwa anthu kulemekeza YehovaNyimbo yokwerera. 1 Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku.
2 Kwezani manja anu kumalo oyera, nimulemekeze Yehova.
3 Yehova, ali mu Ziyoni, akudalitseni; ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.