Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 134:3 - Buku Lopatulika

3 Yehova, ali mu Ziyoni, akudalitseni; ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Yehova, ali m'Ziyoni, akudalitseni; ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Akudalitseni Chauta amene amakhala ku Ziyoni, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitseni kuchokera mʼZiyoni.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 134:3
13 Mawu Ofanana  

Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; chitani ufumu pakati pa adani anu.


Odalitsika inu a kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Thandizo lathu lili m'dzina la Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Yehova adzakudalitsa ali mu Ziyoni; ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.


Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni, amene akhala mu Yerusalemu. Aleluya.


Amene analenga zakumwamba mwanzeru; pakuti chifundo chake nchosatha.


Mwenzi chipulumutso cha Israele chitachokera ku Ziyoni! Pakubweretsa Yehova anthu ake a m'nsinga, pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israele.


likutumizire thandizo lotuluka m'malo oyera, ndipo likugwirizize kuchokera mu Ziyoni;


likumbukire zopereka zako zonse, lilandire nsembe yako yopsereza;


Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele. Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwake;


ndipo chotero Israele yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti, Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi; Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo:


Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa