Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 134:1 - Buku Lopatulika

1 Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Bwerani, mudzatamande Chauta, Inu nonse atumiki a Chauta, inu amene mumatumikira m'Nyumba mwake usiku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Bwerani, mutamande Yehova, inu atumiki onse a Yehova, amene mumatumikira usiku mʼnyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 134:1
32 Mawu Ofanana  

Momwemo iwo ndi ana ao anayang'anira zipata za kunyumba ya Yehova, ndiyo nyumba ya Kachisi, mu udikiro wao.


Ndipo amagona usiku m'zipinda zozinga nyumba ya Mulungu, popeza udikiro wake ndi wao; kuitsegula m'mawa ndi m'mawa ndi kwaonso.


Ndipo awa ndi oimba, akulu a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku ntchito zina; pakuti anali nayo ntchito yao usana ndi usiku.


Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pake, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ake ndi kufukiza zonunkhira.


Ndipo muimirire m'malo opatulika, monga mwa magawidwe a nyumba za makolo za abale anu ana a anthu, akhale nalo onse gawo la nyumba ya makolo ya Alevi.


Ndi Bakibukiya ndi Uni, abale ao, anawayang'anira maulonda.


Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye.


Aleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova.


Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.


Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?


Ndinakondwera m'mene ananena nane, Tiyeni kunyumba ya Yehova.


Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba.


Akadapanda kukhala nafe Yehova, anene tsono Israele;


Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.


Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota.


Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.


Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake.


Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele;


M'mozamamo ndinakufuulirani, Yehova.


Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha.


Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa.


Yehova, kumbukirani Davide kuzunzika kwake konse.


Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!


Wodala munthu amene mphamvu yake ili mwa Inu; mumtima mwake muli makwalala a ku Ziyoni.


Ndipo mukhale pakhomo pa chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga chilangizo cha Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.


zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.


Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino.


Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang'ono ndi aakulu.


Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku mu Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa