Masalimo 2:1 - Buku Lopatulika Aphokoseranji amitundu, nalingiriranji anthu zopanda pake? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aphokoseranji amitundu, nalingiriranji anthu zopanda pake? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bwanji anthu akunja akufuna kuchita chiwembu? Chifukwa chiyani anthu ameneŵa akulingalira zopandapake? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu? Akonzekeranji zopanda pake anthu? |
Musaiwale mau a iwo otsutsana ndi Inu; kusokosera kwa iwo akuukirani Inu kumakwera kosaleka.
Chitani phokoso, anthu inu, koma mudzathyokathyoka; tcherani khutu, inu nonse a maiko akutali; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka.
Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.
Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malovu;
Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira malaya ao; nalamulira kuti awakwapule.
Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.