Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:42 - Buku Lopatulika

42 Pamenepo ndinawapera ngati fumbi la kumphepo; ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Pamenepo ndinawapera ngati fumbi la kumphepo; ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Ndidaŵaperapera ngati fumbi louluka ndi mphepo. Ndimaŵapondereza ngati matope amumseu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Ine ndinawaperesa ngati fumbi lowuluka ndi mphepo. Ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:42
10 Mawu Ofanana  

Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo.


Kodi Mulungu adzamvera kufuula kwake, ikamdzera nsautso?


Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.


Pamenepo adzandiitana, koma sindidzavomera; adzandifunatu, osandipeza ai;


Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala.


Chifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Mowabu adzaponderezedwa pansi m'malo ake, monga udzu uponderezedwa padzala.


Ndani anautsa wina wochokera kum'mawa, amene amuitana m'chilungamo, afike pa phazi lake? Iye apereka amitundu patsogolo pake, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga fumbi kulupanga lake, monga chiputu chouluzidwa ku uta wake.


Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzachita nkhondo, chifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzachitidwa manyazi.


Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa