Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:41 - Buku Lopatulika

41 Anafuula, koma panalibe wopulumutsa; ngakhale kwa Yehova, koma sanawavomereze.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Anafuula, koma panalibe wopulumutsa; ngakhale kwa Yehova, koma sanawavomereze.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Adakuwa kuti ena aŵathandize, koma panalibe woŵapulumutsa. Adalirira Chauta, koma sadaŵayankhe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa. Analirira kwa Yehova koma sanawayankhe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:41
17 Mawu Ofanana  

Kodi Mulungu adzamvera kufuula kwake, ikamdzera nsautso?


Amitundu onse adandizinga, zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.


Adandizinga, inde, adandizinga: Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.


Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.


Pamenepo adzandiitana, koma sindidzavomera; adzandifunatu, osandipeza ai;


Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.


Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzatengera pa iwo choipa, chimene sangathe kuchipulumuka; ndipo adzandifuulira Ine, koma sindidzamvera iwo.


Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi mliri.


Chifukwa chake Inenso ndidzachita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawachitira chifundo Ine; ndipo chinkana afuula m'makutu mwanga ndi mau aakulu, koma sindidzawamvera Ine.


Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.


Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao.


Ndipo kunachitika, monga Iye anafuula, koma iwo sanamvere; momwemo iwo adzafuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu;


Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako;


Ndipo atatero, Yoswa anawakantha nawapha, nawapachika pa mitengo isanu; nalikupachikidwa pa mitengo mpaka madzulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa